8
Kulimbikitsa Zopereka
1 Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. 2 Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. 3 Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, 4 ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. 5 Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu. 6 Choncho tinamupempha Tito kuti atsirize poti nʼkuti atayamba kale ntchito yachisomoyi pakati panu. 7 Popeza pa zinthu zonse munachita bwino, monga pachikhulupiriro, poyankhula, pachidziwitso, pakhama lambiri ndi pachikondi chanu pa ife, onetsetsani kuti muchitenso bwino pachisomo ichi chopereka.
8 Sindikukulamulirani, koma ndikufuna kuona ngati chikondi chanu nʼchoona pofananitsa ndi changu cha anthu ena. 9 Pakuti mukudziwa chisomo cha Ambuye athu Yesu Khristu, kuti ngakhale anali wolemera, koma chifukwa cha inuyo anasanduka wosauka, kuti umphawi wakewo, inuyo mulemere.
10 Ndipo nawa malangizo anga pa zoyenera inu kuchita pa nkhaniyi. Chaka chatha munali oyamba, osati ongofuna kupereka kokha komanso okhala ndi mtima ofuna kupereka. 11 Tsopano tsirizani ntchitoyi, ndipo changu chanu chofunitsitsa kugwira ntchitoyi ndi kuyitsiriza chichitike molingana ndi zimene muli nazo. 12 Ndipo ngati mtima ofunitsitsa ulipo, mphatsoyo imalandiridwa molingana ndi zimene munthuyo ali nazo, osati zimene alibe.
13 Cholinga chathu sikuti tipeputse ena pamene inuyo mukuvutika, koma kuti pakhale kufanana. 14 Zambiri zimene muli nazo pakati panu muthandize nazo osowa, kuti nawonso akadzakhala nazo zambiri adzakuthandizeni pa zosowa zanu. Cholinga nʼkuchita mofanana, 15 monga kwalembedwa kuti, “Iye amene anatola zambiri sizinamutsalireko ndipo amene anatola pangʼono sizinamuchepere.”
Tito Atumidwa ku Korinto
16 Tithokoze Mulungu amene anayika mu mtima wa Tito changu chomwecho chimene ine ndili nacho pa inu. 17 Pakuti Tito sanangovomera kokha pempho lathu, koma yekha anafunitsitsa kwambiri kubwera kwa inu mwa iye yekha. 18 Ndipo tikumutumiza pamodzi ndi mʼbale amene mipingo yonse yamuyamikira chifukwa cha utumiki wake wa Uthenga Wabwino. 19 Chowonjezera china nʼchakuti anasankhidwa ndi mipingo kuti atiperekeze pamene ife tikukapereka zopereka, zimene tikuchita pofuna kupereka ulemu kwa Ambuye mwini ndi kuonetsa kufunitsitsa kwathu pothandiza. 20 Tikufuna kupewa kutikayikira kulikonse za mmene tikuyendetsera mphatso zochulukazi. 21 Pakuti tikuyesetsa kuchita zolondola, osati pamaso pa Ambuye pokha komanso pamaso pa anthu.
22 Kuwonjezera apo, tikuwatumiza pamodzi ndi mʼbale wathu, amene nthawi zambiri watitsimikizira mʼnjira zosiyanasiyana kuti ndi wachangu ndiponso chifukwa ali ndi chikhulupiriro chachikulu mwa inu. 23 Kunena za Tito, ndiye mnzanga ndi wogwira naye ntchito pakati panu. Kunena za abale athu, ndiwo oyimirira mipingo ndi olemekezetsa Khristu. 24 Choncho anthu amenewa atsimikizireni za chikondi chanu ndipo adziwe chifukwa chimene ife timakunyadirani, kuti mipingo yonse iwone chimenechi.