30
Guwa Lansembe Yofukiza
1 Upange guwa lamatabwa amtengo wa mkesha lofukizirapo lubani. 2 Likhale lofanana mbali zonse. Mulitali masentimita 46, mulifupi masentimita 46, ndipo msinkhu masentimita 91. Nyanga zake zipangidwe kumodzi ndi guwalo. 3 Ukute guwa lonse ndi golide wabwino kwambiri, pamwamba pake, mbali zonse zinayi, pamodzi ndi nyanga zake. Ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira guwalo. 4 Upange mphete ziwiri zagolide ndipo uzilumikize ku guwa mʼmunsi mwa mkombero, mphete ziwiri ku mbali zonse ziwiri zoyangʼanana. Mphetozo zizigwira nsichi zonyamulira guwalo. 5 Upange mizati yamtengo wa mkesha ndipo uyikute ndi golide. 6 Uyike guwalo patsogolo pa nsalu yotchinga Bokosi la Chipangano. Apa ndi pamene ndizidzakumana nawe.
7 “Aaroni ayenera kumafukiza lubani wonunkhira pa guwalo mmawa uliwonse. Pamene akukonza nyale zija afukizenso lubani. 8 Aaroni ayenera kufukizanso lubani pamene ayatsa nyale madzulo kuti lubani akhale akuyaka nthawi zonse pamaso pa Yehova kwa mibado imene ikubwera. 9 Pa guwapo usafukize lubani wachilendo kapena kuperekapo nsembe yopsereza kapena nsembe yaufa. Usathire pa guwapo ngakhale nsembe yachakumwa. 10 Aaroni azidzapereka nsembe yopepesera machimo pa nyanga za guwalo kamodzi pa chaka. Mwambowu uzidzachitika pogwiritsa ntchito magazi a nsembe yopepesera machimo, ndipo zizidzachitika mʼmibado yanu yonse. Choncho guwa lansembelo lidzakhala loyera ndi loperekedwa kwa Yehova.”
Za Chopereka Chowombolera Moyo
11 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 12 “Pamene ukuchita kalembera wa Aisraeli, munthu aliyense ayenera kupereka kwa Yehova chowombolera moyo wake pamene akuwerengedwa. Motero mliri sudzabwera pa iwo pamene ukuwawerenga. 13 Izi ndi zimene aliyense wolembedwa mu kawundula ayenera kupereka: theka la sekeli, kutanthauza ndalama zolemera magalamu asanu ndi limodzi malingana ndi kawerengedwe ka ndalama za ku Nyumba ya Mulungu. Paja sekeli imodzi ikulingana ndi magera makumi awiri. Theka la sekeli chidzakhala chopereka cha kwa Yehova. 14 Aliyense wolembedwa mu kawundula amene ali ndi zaka makumi awiri kapena kupitirira ayenera kupereka chopereka kwa Yehova. 15 Anthu olemera asapereke koposa theka la sekeli ndipo osauka asapereke kuchepera theka la sekeli pamene mukupereka nsembe kwa Yehova yowombolera miyoyo yanu. 16 Ulandire ndalama zopepeserazo kuchokera kwa Aisraeli ndipo zigwiritsidwe ntchito ya ku tenti ya msonkhano. Zoperekazi zidzakhala chikumbutso cha Aisraeli pamaso pa Yehova, ndiponso zowombolera miyoyo yanu.”
Za Beseni Losambira
17 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 18 “Upange beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso. Uliyike pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo uthiremo madzi. 19 Aaroni ndi ana ake azisamba mʼmanja ndi kutsuka mapazi awo ndi madzi amenewo. 20 Pamene akulowa mu tenti ya msonkhano, iwo asambe madziwa kuti asafe. Ndiponso pamene akupita kukatumikira ku guwa lansembe ndi kupereka nsembe yopsereza kwa Yehova, 21 azisamba mʼmanja mwawo ndi kutsuka mapazi kuti asadzafe. Limeneli ndi lamulo limene Aaroni, pamodzi ndi ana ndi zidzukulu zake mʼtsogolomo ayenera kumadzalitsatira mpaka muyaya.”
Mafuta Wodzozera
22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, 23 “Utenge zonunkhira bwino kwambiri izi: makilogalamu asanu ndi limodzi a mure wamadzi, makilogalamu atatu a zonunkhira bwino za mtundu wa sinamoni, makilogalamu atatu a nzimbe yonunkhira bwino kwambiri, 24 makilogalamu asanu ndi limodzi a mkesha. Zonsezi zikhale malingana ndi muyeso wa ku Nyumba ya Mulungu. Pakhalenso malita anayi a mafuta a olivi. 25 Ugwiritse ntchito zinthu zimenezi kupanga mafuta opatulika odzozera, mafuta onunkhira, apangidwe ndi mʼmisiri waluso lopanga zonunkhiritsa. Awa adzakhala mafuta opatulika odzozera. 26 Tsono uwagwiritse ntchito podzoza tenti ya msonkhano, Bokosi la Chipangano, 27 tebulo, ndi ziwiya zake zonse, choyikapo nyale ndi zipangizo zake, guwa lofukizirapo lubani, 28 guwa lansembe yopsereza ndi ziwiya zake zonse, ndiponso beseni pamodzi ndi nsichi yake. 29 Zonsezi uzipatule kuti zidzakhale zopatulika, ndipo chilichonse chimene chidzakhudza zimenezi chidzakhala chopatulika.
30 “Udzoze Aaroni ndi ana ake aamuna ndi kuwapatula kuti akhale ansembe onditumikira. 31 Tsono awuze a Israeli kuti, mafuta wodzozera awa adzakhala wopatulika mpaka muyaya. 32 Musadzadzozere munthu wamba mafuta amenewa, ndipo musadzapange mafuta wofanana ndi amenewa. Mafutawa ndi wopatulika ndipo akhale woyera kwa inu. 33 Wina aliyense amene adzapanga mafuta wonunkhira wofanana nawo kapena kudzozera mafutawa munthu wamba osati wansembe ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.”
Za Zofukiza
34 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Tenga muyeso wofanana wa zinthu zonunkhira izi: sitakate, onika, galibanumu pamodzi ndi lubani weniweni. 35 Uziphatikize pamodzi zonsezi ndi kupanga lubani monga amachitira mmisiri wopanga zonunkhira. Athire mchere ndipo akhale woyera ndi wopatulika. 36 Upere gawo lina mosalala kwambiri ndipo utapepo pangʼono ndi kuyika patsogolo pa Bokosi la Chipangano mu tenti ya msonkhano, kumene ine ndidzakumane nawe. Lubani ameneyu kwa inu adzakhala wopatulika kwambiri. 37 Musapange lubani wanu potsatira njira iyi. Lubani yense wopangidwa mwa njira iyi akhale wopatulika, woperekedwa kwa Yehova. 38 Aliyense amene adzapanga wofanana naye kuti asangalale ndi fungo lake ayenera kuchotsedwa pakati pa anthu anzake.”