21
Malamulo a Ansembe
1 Yehova anawuza Mose kuti, “Yankhula ndi ansembe, ana a Aaroni, ndipo uwawuze kuti, ‘Wansembe asadzidetse pokhudza munthu wakufa pakati pa abale ake. 2 Koma akhoza kukhudza thupi lakufa la amayi ake, abambo ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, mchimwene wake, 3 kapena mlongo wake wosakwatiwa amene amadalira iye chifukwa sanakwatiwe. Iye akhoza kudzidetsa pokhudza thupi lakufa la mchemwali wake wosakwatiwa yekha. 4 Koma wansembe asadzidetse chifukwa cha anthu amene ali nawo pa ubale obwera chifukwa cha ukwati.
5 “ ‘Ansembe asamete tsitsi kumutu kwawo kapena mʼmphepete mwa ndevu zawo, kapenanso kudzichekacheka pa thupi lawo. 6 Ayenera kukhala oyera pamaso pa Mulungu wawo ndipo asachititse manyazi dzina la Mulungu wawo. Popeza amapereka nsembe zotentha pa moto kwa Yehova, chakudya cha Mulungu wawo, iwo azikhala woyera.
7 “ ‘Asakwatire akazi amene adzidetsa ndi chiwerewere kapena akazi amene amuna awo awasudzula, chifukwa ansembe ndi oyera pamaso pa Mulungu wawo. 8 Iwo akhale oyera chifukwa amapereka nsembe kwa Mulungu wanu. Muziwaona kuti ndi oyera, popeza Ine Yehova amene ndimawayeretsa ndine woyera, nawonso akhale oyera.
9 “ ‘Ngati mwana wamkazi wa wansembe adziyipitsa pochita zachiwerewere, ndiye kuti iye akuchititsa manyazi abambo ake; mwanayo atenthedwe pa moto.
10 “ ‘Munthu amene ali mkulu wa ansembe pakati pa abale ake, amene anamudzoza pomutsanulira mafuta pamutu pake, ndiponso amene anapatulidwa pomuveka zovala zaunsembe, asalekerere tsitsi lake kapena kungʼamba zovala zake kusonyeza kuti ali pa chisoni. 11 Asalowe mʼnyumba mmene muli munthu wakufa ngakhale womwalirayo ndi amayi ake kapena abambo ake. 12 Asadzidetse potulukira kunja kwa malo opatulika popeza mafuta womupatula kukhala wansembe ali pamutu pake. Ine ndine Yehova.
13 “ ‘Iye akwatire namwali wosadziwa mwamuna. 14 Asakwatire mkazi wamasiye, mkazi wosudzulidwa, kapena mkazi wachiwerewere, koma akwatire namwali wosadziwa mwamuna pakati pa anthu a mtundu wake, 15 kuti mtundu wake usakhale wodetsedwa pakati pa abale popeza ndine Yehova, amene ndimamuyeretsa.’ ”
16 Yehova anawuza Mose kuti, 17 “Muwuze Aaroni kuti, ‘Munthu aliyense mwa zidzukulu zake ku mibado yawo yonse ikubwera akakhala ndi chilema asabwere kudzapereka nsembe kwa Mulungu wake. 18 Munthu aliyense wachilema motere: munthu wakhungu kapena wolumala miyendo, munthu wolumala nkhope kapena waziwalo zambiri, 19 munthu wa phazi lolumala kapena dzanja lolumala, 20 kapena munthu wokhota msana kapena wamfupi kwambiri, kapena wolumala maso, munthu wa nthenda yonyerenyetsa, kapena wamphere, kapenanso wophwanyika mavalo, sayenera kusendera pafupi. 21 Mdzukulu aliyense wa Aaroni wansembe, amene ali ndi chilema asadzayandikire kukapereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Popeza kuti ali ndi chilema, asayandikire kudzapereka nsembe ya chakudya kwa Mulungu wake. 22 Koma iye angathe kudya chakudya chopatulika kwambiri chija, ngakhalenso chakudya chotsala pa nsembe zopatulika. 23 Koma chifukwa cha kulumala kwake, sayenera kuyandikira katani kapena kufika pa guwa kuti angadetse malo anga wopatulika. Ine ndine Yehova, amene ndimawayeretsa.’ ”
24 Choncho Mose anawuza Aaroni ndi ana ake pamodzi ndi Aisraeli onse zimenezi.