4
Haa! Golide wathimbirira,
golide wosalala wasinthikiratu!
Amwazamwaza miyala yokongola ya kumalo opatulika
pamphambano ponse pa mzinda.
 
Haa! Ana a Ziyoni amtengowapatali
amene kale anali ngati golide,
tsopano ali ngati miphika ya dothi,
ntchito ya owumba mbiya!
 
Ngakhale nkhandwe zimapereka bere
kuyamwitsa ana ake,
koma anthu anga asanduka ankhanza
ngati nthiwatiwa mʼchipululu.
 
Lilime la mwana lakangamira kukhosi
chifukwa cha ludzu,
ana akupempha chakudya,
koma palibe amene akuwapatsa.
 
Iwo amene kale ankadya zonona
akupemphetsa mʼmisewu ya mu mzinda.
Iwo amene kale ankavala zokongola
tsopano akugona pa phulusa.
 
Kuyipa kwa anthu anga kunali kwakukulu
kuposa anthu a ku Sodomu,
amene anawonongedwa mʼkamphindi kochepa
popanda owathandiza.
 
Akalonga ake anali owala koposa chisanu chowundana
ndi oyera kuposa mkaka.
Matupi awo anali ofiira kuposa miyala ya rubi,
maonekedwe awo ngati miyala ya safiro.
 
Koma tsopano maonekedwe awo ndi akuda kuposa mwaye;
palibe angawazindikire mʼmisewu ya mu mzinda.
Khungu lawo lachita makwinyamakwinya pa mafupa awo;
lawuma gwaa ngati nkhuni.
 
Amene anaphedwa ndi lupanga aliko bwino kuposa
amene anafa ndi njala;
chifukwa chosowa chakudya cha mʼmunda
iwowa ankafowoka ndi njala mpaka kufa.
 
10 Amayi achifundo afika
pophika ana awo enieni,
ndiwo anali chakudya chawo pamene anthu
anga anali kuwonongeka.
 
11 Yehova wakwaniritsa ukali wake;
wagwetsa pansi mkwiyo wake woopsa.
Ndipo wayatsa moto mʼZiyoni
kuti uwononge maziko ake.
 
12 Mafumu a pa dziko lapansi sanakhulupirire,
kapena wina aliyense wokhala pa dziko lonse,
kuti adani kapena ankhondo akhoza kulowa
pa zipata za Yerusalemu.
 
13 Koma izi zinachitika chifukwa cha kuchimwa kwa aneneri ake
ndi mphulupulu za ansembe ake,
amene ankapha anthu osalakwa pakati pawo.
 
14 Tsopano akungoyendayenda mʼmisewu ya mu mzinda
ngati anthu osaona.
Iwo ndi odetsedwa kwambiri ndi magazi
palibe yemwe angayerekeze nʼkukhudza komwe chovala chawo.
 
15 Anthu akuwafuwulira kuti, “Chokani! Inu anthu odetsedwa!”
“Chokani! Chokani! Musatikhudze ife!”
Akamathawa ndi kumangoyendayenda,
pakati pa anthu a mitundu yonse amati,
“Asakhalenso ndi ife.”
 
16 Yehova mwini wake wawabalalitsa;
Iye sakuwalabadiranso.
Ansembe sakulandira ulemu,
akuluakulu sakuwachitira chifundo.
 
17 Ndiponso maso athu atopa nʼkuyangʼana,
chithandizo chosabwera nʼkomwe,
kuchokera pa nsanja zathu tinadikirira mtundu
wa anthu umene sukanatipulumutsa.
 
18 Anthu ankalondola mapazi athu,
choncho sitikanayenda mʼmisewu yathu mu mzinda.
Chimaliziro chathu chinali pafupi, masiku athu anali owerengeka,
chifukwa chimaliziro chathu chinali chitafika.
 
19 Otilondola akuthamanga kwambiri
kuposa ziwombankhanga mu mlengalenga;
anatithamangitsa mpaka ku mapiri
ndi kutibisalira mʼchipululu.
 
20 Wodzozedwa wa Yehova, mpweya wathu wotipatsa moyo,
anakodwa mʼmisampha yawo.
Tinaganiza kuti tidzakhala pansi pa mthunzi wake
pakati pa mitundu ya anthu.
 
21 Kondwera ndi kusangalala, mwana wamkazi wa Edomu.
Iwe amene umakhala mʼdziko la Uzi.
Koma iwenso chikho chidzakupeza;
udzaledzera mpaka kukhala maliseche.
 
22 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chako chidzatha;
Iye sadzatalikitsa nthawi yako ya ukapolo.
Koma Yehova adzalanga machimo ako, iwe mwana wamkazi wa Edomu,
ndi kuyika poyera mphulupulu zako.