14
Kuyeretsedwa ku Nthenda ya Khate
1 Yehova anawuza Mose kuti, 2 “Malamulo a munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake ndi awa: Abwere naye kwa wansembe. 3 Wansembe atuluke kunja kwa msasa ndipo amuonetsetse wodwalayo. Ngati munthu wakhateyo wachira, 4 wansembe alamule anthu kuti amutengere wodwala woti ayeretsedweyo, mbalame zamoyo ziwiri zomwe Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope. 5 Wansembe alamule anthuwo kuti mbalame imodzi ayiphere mu mʼphika wa dothi pamwamba pa madzi abwino. 6 Kenaka wansembe atenge mbalame yamoyo ija ndi kuyinyika pamodzi ndi nthambi yamkungudza, kansalu kofiirira ndi kanthambi ka hisope kaja mʼmagazi ambalame imene anayiphera pamwamba pa madzi abwino. 7 Wansembe awaze magazi kasanu ndi kawiri pa munthu woti amuyeretse khateyo ndipo alengeze kuti munthuyo ndi woyeretsedwa. Kenaka wansembe awulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo.
8 “Munthu amene wayeretsedwa uja achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe mʼmadzi. Akatero adzakhala woyeretsedwa. Atatha zimenezi munthuyo apite ku msasa wake koma akhale kunja kwa msasawo kwa masiku asanu ndi awiri. 9 Pa tsiku lachisanu ndi chiwiri amete tsitsi lake lonse: amete kumutu, ndevu zake, nsidze zake pamodzi ndi tsitsi lina lonse. Kenaka achape zovala zake ndi kusamba mʼmadzi, ndipo adzakhala woyeretsedwa.
10 “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu munthuyo atenge ana ankhosa aamuna awiri ndi mwana wankhosa wamkazi wa chaka chimodzi. Zonsezi zikhale zopanda chilema. Atengenso chopereka chachakudya cha ufa wosalala wa makilogalamu atatu wosakaniza ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. 11 Wansembe amene ati ayeretse munthu wodwalayo amuyimitse munthuyo ali ndi zopereka zake zonse pamaso pa Yehova pa khomo la tenti ya msonkhano.
12 “Ndipo wansembe atenge mwana wankhosa wamwamuna mmodzi ndi kumupereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta wokwana limodzi mwa magawo atatu a lita. Wansembe aziweyule zonsezi pamaso pa Yehova kuti zikhale chopereka choweyula. 13 Mwana wankhosayo amuphere pa malo amene amaphera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, kutanthauza malo opatulika. Monga zimakhalira ndi chopereka chopepesera machimo, chopereka ichi ndi chake cha wansembe ndipo ndi chopereka choyera kopambana. 14 Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera kupalamula ndi kuwapaka pa msonga pa khutu lakumanja la munthu woti ayeretsedweyo. Apakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi chala chachikulu cha ku phazi lakumanja. 15 Wansembe atengeko mafuta pangʼono, nʼkuwathira mʼdzanja lake lamanzere, 16 aviyike chala chake cha ku dzanja lamanja mʼmafuta amene ali mʼdzanja lamanzerewo, ndi kuwaza mafutawo ndi chala chakecho kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova. 17 Wansembe apake mafuta otsala mʼdzanja lake pa khutu lakumanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Awapakenso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku phazi lakumanja, pamalo pamene anali atapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula paja. 18 Mafuta onse otsala mʼdzanja la wansembe awathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja, ndipo potero adzachita mwambo womupepesera pamaso pa Yehova.
19 “Kenaka wansembe apereke nsembe yopepesera machimo kuti achite mwambo womupepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Atatha kuchita zimenezi, wansembe aphe nyama ya nsembe yopsereza 20 ndi kuyipereka pa guwa, pamodzi ndi nsembe yachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera munthu wodzayeretsedwayo, ndipo adzakhala woyera.
21 “Ngati munthu woti ayeretsedweyo ndi wosauka ndipo sangathe kupeza zinthu zimenezi, apereke mwana wankhosa wamwamuna monga nsembe yopepesera kupalamula ndipo ayiweyule pochita mwambo womupepesera. Aperekenso kilogalamu imodzi ya ufa wosalala osakaniza ndi mafuta kuti ikhale nsembe yachakudya, pamodzi ndi mafuta wokwanira limodzi mwa magawo atatu a lita. 22 Aperekenso njiwa ziwiri kapena mawunda awiri zomwe iye angathe kuzipeza. Imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndi inayo ikhale ya nsembe yopsereza.
23 “Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pa khomo pa tenti ya msonkhano, pamaso pa Yehova kuti munthuyo ayeretsedwe. 24 Wansembe atenge mwana wankhosa wopereka nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule kuti zikhale nsembe yoweyula pamaso pa Yehova. 25 Wansembe aphe nkhosa yopereka nsembe yopepesera kupalamula ndipo atenge magazi ake ndi kuwapaka pa msonga ya khutu lakumanja la munthu amene ayeretsedweyo. Awapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndiponso pa chala chachikulu cha ku phazi lakumanja. 26 Kenaka wansembe athire mafuta mʼdzanja lake lamanzere, 27 ndipo ndi chala chake cha ku dzanja lamanja awaze mafutawo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova. 28 Apakenso mafuta omwewo amene ali mʼdzanja lake lamanja pa msonga ya khutu la kudzanja lamanja la munthu amene akuyeretsedwayo. Apakenso pa chala chachikulu cha phazi lakumanja, pamalo pamene anapakapo magazi a nsembe yopepesera kupalamula. 29 Mafuta onse otsala amene ali mʼdzanja la wansembe awapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo kuti amuchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Yehova. 30 Ndipo munthuyo apereke njiwa ziwiri kapena mawunda ankhunda awiri, molingana ndi mmene anapezeramo, 31 imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo ndipo inayo ikhale ya nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka chachakudya. Akatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu woti ayeretsedwe.
32 “Amenewa ndi malamulo a munthu wakhate amene alibe zinthu zoti apereke pamene akuyeretsedwa.
Za Ndere za Mʼnyumba
33 “Yehova anawuza Mose ndi Aaroni kuti, 34 Mukakalowa mʼdziko la Kanaani limene ndikukupatsani kuti likhale lanu, ndipo Ine ndikakabweretsa ndere zoyanga mʼnyumba mʼdziko limenelo, 35 mwini wake nyumbayo adzapite kwa wansembe ndi kukamuwuza kuti, ‘Ndaona chinthu chooneka ngati ndere mʼnyumba mwanga.’ 36 Tsono wansembe alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse mʼnyumbamo iye asanalowemo ndi kukaonetsetsa ndereyo kuti mʼnyumbamo musapezeke chinthu choti achitchule chodetsedwa. Izi zitachitika, wansembe alowe mʼnyumbamo ndi kukaonamo. 37 Iye aonetsetse nderezo. Tsono akapeza kuti nderezo zili mʼkhoma la nyumba, ndipo ngati zili ndi mawanga obiriwira kapena ofiirira, komanso zikuoneka kuti zalowerera mpaka mʼkati mwa khoma, 38 wansembe atuluke mʼnyumbamo ndi kupita pa khomo, ndipo ayitseke nyumbayo masiku asanu ndi awiri. 39 Pa tsiku la chisanu ndi chiwiri wansembe abwerenso kudzayangʼana mʼnyumbamo. Ngati ndere yafalikira mʼmakoma a nyumbayo, 40 wansembe alamule kuti anthu agumule miyala imene muli nderezo ndipo akayitaye kudzala la kunja kwa mzinda. 41 Wansembe awuze anthu kuti apale makoma onse a mʼkati mwa nyumbayo, ndipo zopalidwazo akazitaye ku malo odetsedwa a kunja kwa mudzi. 42 Tsono anthuwo atenge miyala ina ndi kuyilowetsa mʼmalo mwa miyala imene anagumula ija ndipo atenge dothi latsopano ndi kumata nyumbayo.
43 “Ngati ndere iwonekanso mʼnyumbamo atagumula kale miyala ndiponso atayipala kale ndi kuyimatanso, 44 wansembe apite kukayionetsetsenso ndipo ngati nderezo zafalikira mʼnyumbamo, ndiye kuti ndere zimenezo ndi zoopsa. Nyumba imeneyo ndi yodetsedwa. 45 Agwetse nyumbayo, ndipo miyala yake, matabwa pamodzi ndi dothi lake lonse, zonse akazitaye kudzala lodetsedwa, kunja kwa mzinda.
46 “Aliyense amene alowa mʼnyumbamo itatsekedwa adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo. 47 Munthu amene wagona mʼnyumbamo kapena kudyeramo ayenera kuchapa zovala zake.
48 “Koma ngati pambuyo pa kuyimata, wansembe abwera kudzaonetsetsa mʼnyumbamo napeza kuti ndereyo sinafalikire, iye alengeze kuti nyumbayo ndi yoyeretsedwa, chifukwa ndereyo yatha. 49 Kuti nyumbayo iyeretsedwe, mwini wake atenge mbalame ziwiri, kanthambi kamkungudza, kansalu kofiirira ndi kachitsamba ka hisope. 50 Wansembe aphe mbalame imodzi pamwamba pa madzi abwino mu mʼphika wa dothi. 51 Kenaka atenge kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope, kansalu kofiirira pamodzi ndi mbalame yamoyo ija, zonsezi aziviyike mʼmagazi a mbalame yophedwa ija, ndiponso mʼmadzi abwino aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kawiri 52 Akatero ndiye kuti wayeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi abwino, mbalame yamoyo, kanthambi kamkungudza, kachitsamba ka hisope ndi kansalu kofiirira. 53 Kenaka ayiwulutsire mbalame yamoyo ija kuthengo, kunja kwa mzinda. Pamenepo ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera nyumbayo, ndipo idzakhala yoyeretsedwa.”
54 Amenewa ndiwo malamulo a nthenda ya khate, bala lonyerenyetsa, 55 nguwi za pa zovala, ndere za mʼnyumba, 56 khate la chithupsa, khate la mʼbuko ndi khate la banga 57 kuti mudziwe ngati chinthucho ndi choyeretsedwa kapena chodetsedwa.
Amenewa ndiwo malamulo a nthenda zonse za khate.