MASALIMO. 2. Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu? Akonzekeranji zopanda pake anthu? Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo; ndipo olamulira asonkhana pamodzi kulimbana ndi Ambuye ndi wodzozedwa wakeyo. Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo ndipo titaye zingwe zawo.” Wokhala mmwamba akuseka; Ambuye akuwanyoza iwowo. Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti, “Ine ndakhazikitsa mfumu yanga pa Ziyoni, phiri langa loyera.” Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula: Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga; lero Ine ndakhala Atate ako. Tandipempha, ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako; malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako. Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo; udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.” Kotero, inu mafumu, chenjerani; chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi. Tumikirani Yehova mwa mantha ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera. Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.