MASALIMO. 11. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Mwa Yehova ine ndimathawiramo. Nanga mungathe bwanji kunena kwa ine kuti, “Thawira ku phiri lako ngati mbalame. Pakuti taona oyipa akunga mauta awo; ayika bwino mivi yawo pa zingwe za uta, pobisala pawo kuti alase olungama mtima. Tsono ngati maziko awonongeka, olungama angachite chiyani?” Yehova ali mʼNyumba yake yoyera; Yehova ali pa mpando wake waufumu kumwamba. Iye amayangʼanitsitsa ana a anthu; maso ake amawayesa. Yehova amayesa olungama, koma moyo wake umadana ndi oyipa, amene amakonda zachiwawa. Iye adzakhuthulira pa oyipa makala amoto ndi sulufule woyaka; mphepo yotentha idzakhala yowayenera. Pakuti Yehova ndi wolungama, Iye amakonda chilungamo; ndipo anthu olungama adzaona nkhope yake.