MASALIMO. 19. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Zakumwamba zimalengeza za ulemerero wa Mulungu; thambo limalalikira ntchito za manja ake. Tsiku ndi tsiku zimayankhula mawu ambiri, usiku ndi usiku zimaonetsa poyera nzeru. Palibe kuyankhula, palibe mawu aliwonse; liwu lawo silimveka. Koma uthenga wawo umapita pa dziko lonse lapansi, mawuwo amafika mpaka kumalekezero a dziko lapansi. Dzuwa lili ngati mkwatibwi wobwera kuchokera ku nsanja yake, ngati katswiri wokondwerera kuthamanga pa mpikisano. Limatuluka kuyambira mbali ina ya thambo ndi kuzungulira mpaka mbali inanso; palibe chinthu chotha kupewa kutentha kwake. Lamulo la Yehova ndi langwiro, kutsitsimutsa moyo. Maumboni a Yehova ndi odalirika, amapereka nzeru kwa wopanda nzeru. Malangizo a Yehova ndi olungama, amapereka chimwemwe mu mtima. Malamulo a Yehova ndi onyezimira, amapereka kuwala. Kuopa Yehova ndiye chinthu changwiro, chimakhala mpaka muyaya. Maweruzo a Yehova ndi owona ndipo onse ndi olungama; ndi a mtengowapatali kuposa golide, kuposa golide weniweni; ndi otsekemera kuposa uchi, kuposa uchi wochokera pa chisa chake. Mtumiki wanu amachenjezedwa nawo; powasunga pali mphotho yayikulu. Ndani angathe kudziwa zolakwa zake? Mundikhululukire zolakwa zanga zobisika. Muteteze mtumiki wanunso ku machimo ochita akudziwa; iwo asandilamulire. Kotero ndidzakhala wosalakwa, wopanda mlandu wa tchimo lalikulu. Mawu a mʼkamwa mwanga ndi zolingalira za mu mtima mwanga zikhale zokondweretsa pamaso panu, Inu Yehova, Thanthwe langa ndi Mpulumutsi wanga.