MASALIMO. 82. Salimo la Asafu. Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu; Iye akuweruza pakati pa “milungu.” “Mudzateteza osalungama mpaka liti, ndi kukondera anthu oyipa? Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye; mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika. Landitsani anthu ofowoka ndi osowa; apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa. “Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse. Amayendayenda mu mdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. “Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu, nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’ Koma mudzafa ngati anthu wamba; mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.” Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi, pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.