MASALIMO. 101. Salimo la Davide. Ndidzayimba za chikondi ndi chiweruzo chanu cholungama; kwa Inu Yehova ndidzayimba matamando. Ndidzatsata njira yolungama; nanga mudzabwera liti kwa ine? Ndidzayenda mʼnyumba mwanga ndi mtima wosalakwa. Sindidzayika chinthu chilichonse choyipa pamaso panga. Ine ndimadana ndi zochita za anthu opanda chikhulupiriro; iwo sadzadziphatika kwa ine. Anthu a mtima wokhota adzakhala kutali ndi ine; ine sindidzalola choyipa chilichonse kulowa mwa ine. Aliyense wosinjirira mnansi wake mseri ameneyo ndidzamuletsa; aliyense amene ali ndi maso amwano ndi mtima wodzikuza, ameneyo sindidzamulekerera. Maso anga adzakhala pa okhulupirika mʼdziko, kuti akhale pamodzi ndi ine; iye amene mayendedwe ake ndi wosalakwa adzanditumikira. Aliyense wochita chinyengo sadzakhala mʼnyumba mwanga. Aliyense woyankhula mwachinyengo sadzayima pamaso panga. Mmawa uliwonse ndidzatontholetsa anthu onse oyipa mʼdziko; ndidzachotsa aliyense wochita zoyipa mu mzinda wa Yehova.