MASALIMO. 110. Salimo la Davide. Yehova akuwuza Mbuye wanga kuti, “Khala ku dzanja langa lamanja mpaka nditasandutsa adani ako kukhala chopondapo mapazi ako.” Yehova adzakuza ndodo yamphamvu ya ufumu wako kuchokera mʼZiyoni; udzalamulira pakati pa adani ako. Ankhondo ako adzakhala odzipereka pa tsiku lako la nkhondo. Atavala chiyero chaulemerero, kuchokera mʼmimba ya mʼbandakucha, udzalandira mame a unyamata wako. Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo ake: “Ndiwe wansembe mpaka muyaya monga mwa unsembe wa Melikizedeki.” Ambuye ali kudzanja lako lamanja; Iye adzaponda mafumu pa tsiku la ukali wake. Adzaweruza anthu a mitundu ina, adzadzaza dziko lapansi ndi mitembo ndipo adzaphwanya olamulira a pa dziko lonse lapansi. Iye adzamwa mu mtsinje wa mʼmbali mwa njira; choncho adzaweramutsa mutu wake.