MASALIMO. 111. Tamandani Yehova. Ndidzathokoza Yehova ndi mtima wanga wonse mʼbwalo la anthu olungama mtima ndi pa msonkhano. Ntchito za Yehova nʼzazikulu; onse amene amakondwera nazo amazilingalira. Zochita zake ndi za ulemerero ndi zaufumu, ndipo chilungamo chake ndi chosatha. Iye wachititsa kuti zodabwitsa zake zikumbukirike; Yehova ndi wokoma mtima ndi wachifundo. Amapereka chakudya kwa amene amamuopa Iye; amakumbukira pangano lake kwamuyaya. Waonetsa anthu ake mphamvu ya ntchito zake, kuwapatsa mayiko a anthu a mitundu ina. Ntchito za manja ake ndi zokhulupirika ndi zolungama; malangizo ake onse ndi odalirika. Malamulo ndi okhazikika ku nthawi za nthawi, ochitidwa mokhulupirika ndi molungama. Iyeyo amawombola anthu ake; anakhazikitsa pangano lake kwamuyaya dzina lake ndi loyera ndi loopsa. Kuopa Yehova ndicho chiyambi cha nzeru; onse amene amatsatira malangizo ake amamvetsa bwino zinthu. Iye ndi wotamandika mpaka muyaya.