MASALIMO. 121. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Ndikweza maso anga ku mapiri; kodi thandizo langa limachokera kuti? Thandizo langa limachokera kwa Yehova, wolenga kumwamba ndi dziko lapansi. Sadzalola kuti phazi lako literereke; Iye amene amakusunga sadzawodzera. Taonani, Iye amene amasunga Israeli sadzawodzera kapena kugona. Yehova ndiye amene amakusunga; Yehova ndiye mthunzi wako ku dzanja lako lamanja. Dzuwa silidzakupweteka nthawi ya masana, kapena mwezi nthawi ya usiku. Yehova adzakuteteza ku zoyipa zonse; adzasunga moyo wako. Yehova adzayangʼanira kutuluka kwako ndi kulowa kwako; kuyambira tsopano mpaka muyaya.