MASALIMO. 124. Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, anene tsono Israeli, akanapanda kukhala mbali yathu Yehova, potiwukira anthuwo, iwo atatipsera mtima, akanatimeza amoyo; chigumula chikanatimiza, mtsinje ukanatikokolola, madzi a mkokomo akanatikokolola. Atamandike Yehova, amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo. Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame yokodwa mu msampha wa mlenje; msampha wathyoka, ndipo ife tapulumuka. Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.