MASALIMO. 128. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Odala ndi onse amene amaopa Yehova, amene amayenda mʼnjira zake. Udzadya chipatso cha ntchito yako; madalitso ndi chuma zidzakhala zako. Mkazi wako adzakhala ngati mpesa wobereka mʼkati mwa nyumba yako; ana ako adzakhala ngati mphukira za mitengo ya olivi kuzungulira tebulo lako. Ameneyu ndiye munthu wodalitsidwa amene amaopa Yehova. Yehova akudalitse kuchokera mʼZiyoni masiku onse a moyo wako; uwone zokoma za Yerusalemu, ndipo ukhale ndi moyo kuti udzaone zidzukulu zako. Mtendere ukhale ndi Israeli.