MASALIMO. 129. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga,” anene tsono Israeli; “Andizunza kwambiri kuyambira ubwana wanga, koma sanandipambane. Anthu otipula analima pa msana panga ndipo anapangapo mizere yayitali: Koma Yehova ndi wolungama; Iye wandimasula ku zingwe za anthu oyipa.” Onse amene amadana ndi Ziyoni abwezedwe pambuyo mwamanyazi. Akhale ngati udzu womera pa denga la nyumba, umene umafota usanakule; sungadzaze manja a owumweta kapena manja a omanga mitolo. Odutsa pafupi asanene kuti, “Dalitso la Yehova lili pa inu; tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”