MASALIMO. 134. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu. Bwerani, mutamande Yehova, inu atumiki onse a Yehova, amene mumatumikira usiku mʼnyumba ya Yehova. Kwezani manja anu mʼmalo opatulika ndipo mutamande Yehova. Yehova wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitseni kuchokera mʼZiyoni.