MASALIMO. 149. Tamandani Yehova. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, matamando ake mu msonkhano wa oyera mtima. Israeli asangalale mwa mlengi wake; anthu a ku Ziyoni akondwere mwa Mfumu yawo. Atamande dzina lake povina ndi kuyimbira Iye nyimbo ndi tambolini ndi pangwe. Pakuti Yehova amakondwera ndi anthu ake; Iye amaveka chipulumutso odzichepetsa. Oyera mtima asangalale mu ulemu wake ndi kuyimba mwachimwemwe pa mabedi awo. Matamando a Mulungu akhale pakamwa pawo, ndi lupanga lakuthwa konsekonse mʼmanja mwawo, kubwezera chilango anthu a mitundu ina, ndi kulanga anthu a mitundu yonse, kumanga mafumu awo ndi zingwe, anthu awo otchuka ndi unyolo wachitsulo, kuchita zimene zinalembedwa zotsutsana nawo Uwu ndi ulemerero wa oyera mtima ake onse. Tamandani Yehova.