5
Yesu Ayitana Ophunzira Oyamba
Tsiku lina Yesu anayima mʼmbali mwa nyanja ya Genesareti, gulu la anthu litamuzungulira likumvetsera mawu a Mulungu. Iye anaona mabwato awiri ali mʼmphepete mwa nyanja, asodzi amene ankachapa makhoka awo atawasiya pamenepo. Iye analowa mʼbwato limodzi limene linali la Simoni, ndi kumupempha kuti alikankhire mʼkati mwa nyanja pangʼono. Kenaka Iye anakhala pansi nayamba kuphunzitsa anthu ali mʼbwatomo.
Atatha kuyankhula anati kwa Simoni, “Kankhirani kwa kuya ndipo muponye makhoka kuti mugwire nsomba.”
Simoni anayankha kuti, “Ambuye, tagwira ntchito molimbika usiku wonse, koma sitinagwire kanthu. Koma pakuti mwatero, ndiponya makhoka.”
Atachita izi, anagwira nsomba zambiri kotero kuti makhoka awo anayamba kungʼambika. Choncho anakodola anzawo a bwato linalo kuti abwere ndi kuwathandiza, ndipo anabwera nadzaza mabwato onse awiri mpaka kuyamba kumira.
Simoni Petro ataona izi, anagwa pa mawondo a Yesu nati, “Chokani kwa ine Ambuye: Ine ndine munthu wochimwa!” Iye ndi anzake onse anadabwa ndi nsomba zimene anagwira, 10 chimodzimodzinso Yakobo ndi Yohane, ana a Zebedayo, anzake a Simoniyo.
Kenaka Yesu anati kwa Simoni, “Musachite mantha; kuyambira tsopano ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 11 Kenaka anakokera mabwato awo ku mtunda, nasiya zonse namutsata Iye.
Yesu Achiritsa Munthu Wakhate
12 Yesu ali ku mudzi wina, munthu amene anali ndi khate thupi lonse anabwera kwa Iye. Munthuyo ataona Yesu, anagwa chafufumimba ndipo anamupempha Iye kuti, “Ambuye, ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”
13 Yesu anatambasula dzanja lake namukhudza munthuyo. Iye anati, “Ine ndikufuna, yeretsedwa!” Ndipo nthawi yomweyo khate lake linachoka.
14 Kenaka Yesu anamulamula kuti, “Usawuze wina aliyense, koma pita, kadzionetse kwa wansembe ndi kukapereka nsembe zimene Mose anakulamulirani za kuyeretsedwa kwanu monga umboni kwa iwo.”
15 Koma mbiri yake inafalikirabe kwambiri kotero kuti magulu a anthu anabwera kudzamvetsera ndi kuti achiritsidwe ku matenda awo. 16 Koma Yesu nthawi zambiri ankachoka kupita ku malo a yekha kukapemphera.
Yesu Achiritsa Wofa Ziwalo
17 Tsiku lina pamene ankaphunzitsa, Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, amene anachokera ku midzi yonse ya Galileya ndi ku Yudeya ndi Yerusalemu, anakhala pansi pomwepo. Ndipo mphamvu ya Ambuye inalipo yakuti Iye achiritse odwala. 18 Amuna ena anabwera atanyamula munthu wofa ziwalo pa mphasa ndipo anayesa kumulowetsa mʼnyumba kuti amugoneke pamaso pa Yesu. 19 Atalephera kupeza njira yochitira zimenezi chifukwa cha gulu la anthu, anakwera naye pa denga ali pa mphasa pomwepo ndi kumutsitsira mʼkati pakati pa gulu la anthu, patsogolo penipeni pa Yesu.
20 Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anati, “Mnzanga, machimo ako akhululukidwa.”
21 Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo anayamba kuganiza mwa iwo okha kuti, “Kodi munthu uyu ndi ndani amene ayankhula zamwano? Kodi ndani amene angakhululukire machimo kupatula Mulungu?”
22 Yesu anadziwa zomwe iwo amaganiza ndipo anafunsa kuti, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukuganiza zimenezi mʼmitima mwanu? 23  Kodi chapafupi ndi chiti: kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka ndipo yenda?’24  Koma kuti inu mudziwe kuti Mwana wa Munthu ali ndi ulamuliro pa dziko lapansi wokhululukira machimo, Iye anati kwa munthu wofa ziwaloyo, “Ine ndikuwuza iwe kuti, ‘Imirira, nyamula mphasa ndipo uzipita kwanu.’ ” 25 Nthawi yomweyo anayimirira patsogolo pawo, nanyamula mphasa yake ndipo anapita kwawo akuyamika Mulungu. 26 Aliyense anadabwa ndi kuchita mantha ndipo anayamika Mulungu. Iwo anadabwa kwambiri ndipo anati, “Lero taona zinthu zosayiwalika.”
Kuyitanidwa kwa Levi
27 Zitatha izi, Yesu anachoka ndipo anaona wolandira msonkho dzina lake Levi atakhala mʼnyumba ya msonkho. Yesu anati kwa iye, “Nditsate Ine.” 28 Ndipo Levi anayimirira, nasiya zonse ndi kumutsata Iye.
29 Kenaka Levi anakonzera Yesu phwando lalikulu ku nyumba yake ndipo gulu lalikulu la amisonkho ndi ena ankadya naye pamodzi. 30 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amene anali a gulu lawo anadandaula kwa ophunzira ake, “Kodi ndi chifukwa chiyani mukudya ndi kumwa pamodzi ndi amisonkho ndi ochimwa?”
31 Yesu anawayankha kuti, “Amene sakudwala safuna singʼanga, koma odwala. 32  Ine sindinabwere kudzayitana olungama, koma ochimwa kuti atembenuke mtima.”
Yesu Afunsidwa za Kusala Kudya
33 Iwo anati kwa Iye, “Ophunzira a Yohane amasala kudya ndi kupemphera kawirikawiri, monganso ophunzira a Afarisi, koma anu amangodya ndi kumwa.”
34 Yesu anawayankha kuti, “Kodi alendo a mkwati angasale kudya pamene mkwati ali pakati pawo? 35  Koma nthawi ikubwera pamene mkwati adzachotsedwa pakati pawo. Masiku amenewo adzasala kudya.”
36 Iye anawawuza fanizo ili: “Palibe amene amangʼamba chigamba kuchokera pa chovala chatsopano ndi kuchisokerera pa chakale. Ngati atatero, ndiye kuti adzangʼamba chovala chatsopanocho, ndipo chigamba chochokera pa chovala chatsopano chija sichidzagwirizana ndi chakale. 37  Ndipo palibe amene amakhuthulira vinyo watsopano mʼmatumba a vinyo akale. Ngati atatero, vinyo watsopanoyo adzaphulitsa zikopazo, vinyo adzatayika ndipo zikopa za vinyozo zidzawonongeka. 38  Ayi, vinyo watsopano ayenera kuthiridwa mʼmatumba a vinyo azikopa zatsopano. 39  Ndipo palibe amene atamwa vinyo wakale amafuna watsopano, pakuti amati, ‘Wakale ndi okoma.’ ”