6
Yesu Mbuye wa Sabata
Tsiku lina la Sabata Yesu ankadutsa mʼminda yatirigu, ndipo ophunzira ake anayamba kubudula ngala zatirigu, namazifikisa mʼmanja mwawo ndi kumadya. Ena mwa Afarisi anafunsa kuti, “Kodi nʼchifukwa chiyani mukuchita zosaloledwa pa tsiku la Sabata?”
Yesu anawayankha iwo kuti, “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita pamene iye ndi anzake anali ndi njala? Iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo atatenga buledi wopatulika anadya amene ndi ololedwa kudya ansembe okha. Ndipo anaperekanso wina kwa anzake.” Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu ndi Ambuye wa Sabata.”
La Sabata lina Iye analowa mʼsunagoge kukaphunzitsa ndipo mʼmenemo anapeza munthu wadzanja lolumala. Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo ankamuyangʼana kuti apeze chifukwa Yesu, choncho anamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati Iye akanamuchiritsa pa Sabata. Koma Yesu anadziwa zimene ankaganiza ndipo anati kwa munthu wadzanja lolumalayo, “Tanyamuka ndipo uyime patsogolo pa onsewa.” Choncho iye ananyamuka nayima pamenepo.
Kenaka Yesu anawawuza kuti, “Ndikufunseni, kodi chololedwa pa Sabata ndi chiti: kuchita chabwino kapena kuchita choyipa, kupulumutsa moyo kapena kuwononga?”
10 Iye atawayangʼana onsewo, anati kwa munthuyo, “Wongola dzanja lako.” Iye anaterodi, ndipo dzanja lake linachiritsidwa. 11 Koma iwo anapsa mtima nayamba kukambirana wina ndi mnzake chomwe akanamuchitira Yesu.
Atumwi Khumi ndi Awiri
12 Tsiku lina, masiku amenewo, Yesu anapita ku phiri kukapemphera ndipo anakhala usiku wonse akupemphera kwa Mulungu. 13 Kutacha, anayitana ophunzira ake ndipo anasankha khumi ndi awiri a iwo amene anawayika kukhala atumwi: 14 Simoni (amene anamutcha Petro), mʼbale wake wa Andreya, Yakobo, Yohane, Filipo, Bartumeyu, 15 Mateyu, Tomasi, Yakobo mwana wa Alufeyo, Simoni amene amatchedwa Zaleti, 16 Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikarioti amene anamupereka.
Madalitso ndi Tsoka
17 Iye anatsika pamodzi ndi atumwiwo ndipo anayima pamalo athyathyathya. Gulu lalikulu la ophunzira ake, gulu lalikulu la anthu ochokera ku Yudeya konse, ku Yerusalemu ndi ochokera mʼmphepete mwa nyanja ya Turo ndi Sidoni anali pomwepo. 18 Iwo anabwera kudzamvetsera ndi kuchiritsidwa ku matenda awo. Osautsidwa ndi mizimu yoyipa anachiritsidwa, 19 ndipo anthu ankayesetsa kuti amukhudze chifukwa mphamvu imatuluka mwa Iye ndi kuchiritsa onse.
20 Akuyangʼana ophunzira ake, Iye anati,
“Odala ndinu amene ndi osauka,
chifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.
21  Inu amene mukumva njala tsopano, ndinu odala
chifukwa mudzakhutitsidwa.
Inu amene mukulira tsopano, ndinu odala
chifukwa mudzasekerera.
22  Ndinu odala, anthu akamakudani,
kukusalani ndi kukunyozani
ndi kumayipitsa dzina lanu chifukwa cha Mwana wa Munthu.
23  “Nthawi imeneyo sangalalani ndipo lumphani ndi chimwemwe chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba. Pakuti ndi zomwezonso zimene makolo awo anachitira aneneri.
24  “Ndinu atsoka, anthu olemera,
popeza mwalandiriratu zokusangalatsani.
25  Tsoka inu amene mukudya bwino tsopano,
chifukwa mudzakhala ndi njala.
Ndinu atsoka, amene mukusekerera tsopano,
chifukwa mudzabuma ndi kulira.
26  Ndinu atsoka, anthu akamakuyamikirani,
popeza makolo anu anawachitira aneneri onama zomwezi.”
Kukonda Adani
27  “Koma Ine ndikuwuza inu amene mukundimva: Kondani adani anu, chitirani zabwino amene amakudani. 28  Dalitsani amene amakutembererani, apempherereni amene amakusautsani. 29  Ngati wina akumenyani patsaya limodzi mupatseninso tsaya linalo. Ngati wina akulanda mwinjiro wako, umulole atenge ndi mkanjo omwe. 30  Mupatseni aliyense amene akupemphani kanthu ndipo ngati wina atenga chinthu chanu, musamulamule kuti akubwezereni. 31  Inu muwachitire anthu ena, zomwe mukanafuna kuti iwo akuchitireni.
32  “Ngati mukonda okhawo amene amakukondani, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amakonda amene amawakondanso. 33  Ndipo ngati muchita zabwino kwa amene ndi abwino kwa inu, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amachita izi. 34  Ndipo ngati mukongoza amene mukuyembekeza kuti abweza, mwapindula chiyani? Ngakhale ‘ochimwa’ amabwereketsa kwa ochimwa anzawo, ndipo amayembekezera kubwezeredwa zonse. 35  Koma kondani adani anu, achitireni zabwino, akongozeni koma osayembekezera kulandira kanthu. Pamenepo mphotho yanu idzakhala yayikulu ndipo inu mudzakhala ana a Wammwambamwamba, chifukwa ndi wokoma mtima kwa anthu osayamika ndi oyipa. 36  Khalani achifundo, monga momwe Atate anu ali achifundo.”
Za Kuweruza Ena
37  “Musaweruze, ndipo inu simudzaweruzidwa. Musatsutse ndipo inu simudzatsutsidwa. Khululukirani ena ndipo mudzakhululukidwa. 38  Perekani ndipo mudzapatsidwa. Adzakupatsani mʼthumba mwanu muyeso wabwino, wotsenderezeka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Pakuti muyeso umene mumagwiritsa ntchito, ndi omwewo adzakuyeserani.”
39 Iye anawawuzanso fanizo ili, “Kodi munthu wakhungu angatsogolere munthu wakhungu mnzake? Kodi onse sadzagwera mʼdzenje? 40  Wophunzira sangapose mphunzitsi wake, koma yense amene waphunzitsidwa bwinobwino adzakhala ngati mphunzitsi wake.
41  “Kodi ndi chifukwa chiyani mumaona kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu ndi kusasamala mtengo uli mʼdiso mwanu? 42  Kodi munganene bwanji kwa mʼbale wanu kuti, ‘Mʼbale nʼtakuchotsa kachitsotso mʼdiso mwako,’ pamene inu eni ake mukulephera kuona mtengo uli mʼdiso mwanu? Inu achiphamaso, yambani mwachotsa mtengo uli mʼdiso mwanu, ndipo kenaka mudzaona bwinobwino ndi kuchotsa kachitsotso mʼdiso la mʼbale wanu.”
Mtengo ndi Zipatso Zake
43  Palibe mtengo wabwino umene umabala chipatso choyipa, kapena mtengo oyipa umene umabala chipatso chabwino. 44  Mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake. Anthu sathyola nkhuyu pa mtengo waminga, kapena mphesa pa nthungwi. 45  Munthu wabwino amatulutsa zinthu zabwino zosungidwa mu mtima mwake, koma munthu oyipa amatulutsa zinthu zoyipa zosungidwa mu mtima mwake. Pakamwa pake pamayankhula zimene zadzaza mu mtima mwake.
Womanga Nyumba Wanzeru ndi Wopusa
46  “Kodi nʼchifukwa chiyani munditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye’ koma simuchita zimene Ine ndinena? 47  Ine ndidzakuonetsani mmene alili munthu amene amabwera kwa Ine ndi kumva mawu anga ndi kuwachita. 48  Iye ali ngati munthu womanga nyumba, amene anakumba mozama nayika maziko ake pa mwala. Madzi osefukira atabwera ndi mphamvu, nawomba nyumbayo koma sinagwedezeka, chifukwa anayimanga bwino. 49  Koma amene amamva mawu anga koma osawachita, akufanana ndi munthu amene anamanga nyumba yake koma yopanda maziko. Nthawi yomwe madziwo anawomba nyumbayo, inagwa ndipo inawonongekeratu.”